🐝 IndabaX Malawi 2025

Mkumano wa Mzika, a Katswiri a  za Sayansi ku Zokambirana Zoteteza ndi Kubwezeretsa Chilengedwe Pogwiritsa ntchito Njira za Makono

English version

Tsiku: 2-3 Oct 2025 (to be confirmed)
Malo: ODeL Malawi University of Business and Applied Sciences, Blantyre, Malawi

Mkumano wa chaka chino ukubweretsa pamodzi  zotumphuka ku kafukufuku ochokera kwa a katswiri a sayansi, adindo a boma komanso akuluakulu a za malamulo ndi mzika kuti agawane nzeru ndi kumvetsa bwino zokhudza kusamala ndi kubwezeretsa chilengedwe m’Malawi.

Mvetserani za kumkumano wa Indabax 2025 mwachidule.
Listen to a summary (English)
Go to the English version here.

Mkumanowu ukuzindira kuti zamoyo zonse, anthu, nyama ndi zomera, zimakhala modalirana posatengera kumene zimakhala, kaya ndi kumidzi, ku mizinda kapena kutchire. Choncho kusintha kulikonse komwe kungachitike pamalo pomwe pali chilengedwe kumabweretsa zotsatira pamtundu uli onse wa zamoyozi.

Pamene chilengedwe chikumasamalidwa n’kumachita bwino phindu lake limakhala lachionekere popeza: 

  • Kupezeka kwa mpweya wabwino ndi madzi aukhondo kumakhalapo, chuku chimafalika popanda vuto, nyengo imakhala yodalirika ndipo timatetezeka ku matenda. 
  • Mmidzimu chilengedwe chimatithandiza ku ulimi, chimatipatsa mankhwala a zitsamba, nsomba ngati chakudya pomwe zomera zina za kuthengo zimatipindulitsa m’njira zambiri.
  • Pomwe mmizindamu zachilengedwe zikumatithandiza malo athu amene tikukhala kuti azikhala ofunda, zimachepetsa vuto la kusefukira kwa madzi komanso kuthandizira pamoyo wathanzi.

Koma pamene chilengedwe chaonongedwa ndipo chasowa, thengo lawotchedwa, mitengo yadulidwa mosaibwezeretsa, nyama zikuphedwa chisawawa, zinyalala tataya mosasamala, tawononga pogwiritsa ntchito za chilengedwe mopyola muyezo zotsatira zake nzambiri: 

  • Zomera zobiriwira zimakhala zochepa choncho mpweya wabwino umasowa. 
  • Ubale ndi kulumikizana kwa za chilengedwe zimasokonekera, 
  • Nyengo siipanganika choncho ulimi siudalilika
  • Chakudya chimasowa ndipo njala imadza mdziko zomwe zimadzetsa kunyentchera ndipo matenda amafala mosavuta.
  • Chiopsezo cha kukokoloka kwa nthaka chimakhala chachikulu.
  • Anthu okhala m’mizinda amavutika kupeza chakudya chabwino, 
  • Nyengo yotentha imadza choncho zomera zina zimafota nafa,
  • Kukokoloka kwa nthaka kumachuluka, 
  • Zomera zobiriwira zimakhala zochepa choncho mpweya wabwino umasowa. 

Tikukumemani kuti mudzakhale nafe ndikutenga nawo gawo nkumagawana maganizo pa mkumanowu.
Kodi ndinu ophunzira msukulu ya ukachenjede kapena munamaliza ndipo mukugwira ntchito, kapena ndinu a m’mabungwe a za kafukufuku kapena ndinu a dindo opanga ziganizo ndi malamulo m’boma?
Chonde perekani maganizo anu kapena a gulu lanu ndipo mufotokoze ndondomeko zomwe mwakonza.

Chiyembekezo chathu
Kudzakhala mphoto zosiyanasiyana pa gawo lililonse ku mkumanoku, koma izi tidzazilongosola bwino mtsogolo muno.
Tiimbireni pamene mukafuna kudziwa zambiri za mkumanowu.

Pamene tikukhulupirira kuti inu mutenga nawo mbali, ife tikuyembekezera mfundo zotsatirazi kuti zikhalamo m’maganizo amene mungatigawire, angakhale kuti mfundo zili m’munsizi si mapeto a zonse komabe maganizo anu afanane ndi awa:

  1. Zonse zokhudza anthu: kusamala madzi ndi malo okhala.
  2. Zonse zokhudza ma failo: m’ndandanda wa zithu zomwe zasungidwa mmakina a kompyuta.
  3. Zonse zokhudza njira za makono za AI
  4. Njira zofalitsira mauthengawo.

KUTENGA NAWO MBALI

Ngati muli ndi chidwi chotenga nawo mbali, chitani izi:

Titumizireni ganizo lanu lofuna kutenga nawo mbali pasanafike pa 10 June 2025.
Ndipo tsiku lotsiriza kulandira maganizo anu ndi pa 10 July 2025.

Tumizazani izi pamodzi foni yanu ku email iyi: indabax@mubas.ac.mw

Nthawi zina munthu umatha kusowa poyambira, choncho ife tikuti mkumano wa indabax Malawi 2025 ndi mtanga wodzadza ndi mwai wapadera komwe mutha kuphunzirako zambiri zomwe zina zinatsindikizidwa kale koma mwina anthu ambiri sakuzidziwa komanso komwe utha kukatolako  maluso atsopano okhudza za chilengedwe za moyo ndi malo awo. 

Tili ndi cholinga chodzagawana nanu ntchito pa zinthu zina koma izi tidzasowa maganizo anu. 

Chonde ngati muli ndi chidwi pa izi, tilembereni ku email yathu iyi indabax@mubas.ac.mw

Kodi chilengedwe ndi chani?

Chilengedwe amene ali mawu achidule m’malo mwa mawu akuti Zamoyo zosiyanasiyana chimatanthauza kusiyanasiyana ndi kusinthasintha kwa zinthu zonse zamoyo padziko lapansi. Izi zikuphatikizapo:

  1. Kusiyanasiyana kwa majini – kusiyanasiyana kwa majini m’kati mwa mitundu (mwa chitsanzo, mitundu yosiyanasiyana ya agalu kapena mitundu ya zomera ndi mbewu),
  2. Kusiyanasiyana kwa mitundu – mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo zomwe zili m’malo okhala kapena chilengedwe (monga mbalame, tizilombo, nyama zoyamwitsa, ndi zomera),
  3. Kusiyanasiyana kwa chilengedwe – mitundu yosiyanasiyana ya zachilengedwe (mwa  chitsanzo, nkhalango, madambo, matanthwe a Korolo, zipululu).

Zamoyo zosiyanasiyana ndizofunika kuti chilengedwe chikhale chokhazikika, chikhale cholimba, komanso kupereka chithandizo chachilengedwe monga chakudya, mankhwala, madzi aukhondo, ndi mpweya.

Kodi AI ndi chiyani? Ndipo ndi mtundu wanji wa AI womwe mkumanowu udzatakasule?

Artificial Intelligence (AI) imatanthawuza makina apakompyuta omwe amatha “kuganiza” ndikupanga ziganizo monga anthu – kuphatikizapo kuzindikira maonekedwe kapena zinthu mu zithunzi kapena kulosera za kusintha pa chilengedwe. Mkumanowu uyang’ana kwambiri Machine Learning (ML), womwe ndi mtundu wa AI umene umaphunzira machitidwe kuchokera kuma failo osungidwa mu kompyuta kuti uthetse mavuto a mdziko komanso kuunika ndi kuzindikira zinthu zakutali. Komabe, matekinoloje ena a pakompyuta monga kupanga mapu, kulongosola zithunzi, ndi kusonkhanitsa ma failo amu kompyuta , nako ndi kofunikira.

Zida za AI zimathandiza asayansi, osamalira zachilengedwe, komanso anthu ammadera kupanga ziganizo zabwino zotetezera chilengedwe ndi mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo. Mwachitsanzo, ML ingagwiritsidwe ntchito pozindikira nyama zomwe zili pachiopsezo pogwiritsa ntchito ma kamela, kuzindikila malo omwe padulidwa mitengo pogwiritsa ntchito zithunzi zojambulidwa ndi makina a satellite,  kapena kulosera momwe nyengo kapena kusintha kwanyengo kungakhudzire zomera ndi nyama.

Mwachitsanzo, AI ingagwiritsidwe ntchito poyerekezera kapena kuyeza mlingo wakudulidwa kwa mitengo kuchokera pazithunzi za satellite. Zida ngati Global Forest Watch zimagwiritsa ntchito AI posanthula ma failo a makina a satellite ndikuona kudula kosaloledwa kwa mitengo kapena kaonongeke ka nkhalango mu nthawi yosalekeza zimene zimathandiza amalamulo kuchitapo kanthu mwachangu.

Ku labu yathu ya kafukufuku, Kuyesera AI, posachedwapa tapanga ma failo okhala ndi zithunzi za satellite kuti tizindikire kuwonongeka kwa nyumba komwe kumachitika chifukwa cha kusefukira  kwa madzi mwadzidzidzi ku Blantyre. mwBTFreddy ilipo ndipo titha kuthandizana pogwiritsa ntchito ma failowa pa mayesero a Machine Learning.

AI ikhoza kuthandizira kusanthula zithunzi za satellite kapena zam’mlengalenga pofuna kuzindikira ndikuwunika kugawidwa kwa mapaki, minda, ndi madenga obiriwira m’mizinda zimene zimathandizira kupangidwa kwabwino kwamatauni motsatana ndi chilengedwe. AI imatha kuzindikira kulira kwa mbalame, achule, kapena mileme pogwiritsa ntchito zida zotapila mawu. Izi zimathandiza asayansi kuyang’anira zamoyo za m’nkhalango popanda kufunikira kukhalapo mwakuthupi. Mitundu ya ML imatha kuphatikiza ma failo okhudzana ndi nyengo, malo, ndi mawonekedwe a zamoyo kuti alosere komwe nyama kapena zomera zina zitha kukhala – komanso momwe zingasinthire ndi kusintha kwa nyengo.

Zitsanzo za Sayansi Yochitidwa ndi Nzika

Kufotokoza nkhani

Kufotokozera nkhani ndi chida champhamvu cholumikizirana, makamaka chikaphatikizidwa ndi makanema osiyanasiyana monga zolemba, zowonera, zomvera, ndi mamapu. Zamoyo zosiyanasiyana nthawi zambiri zimamveka ngati nkhani yakutali, ya sayansi, koma kufotokoza nkhani kumapweketsa zinthu zovuta, kuzisintha kukhala nkhani zomveka komanso zolumikizanika. Nkhani zimatha kulumikiza zinthu zamoyo zosiyanasiyana ndi zochitika za tsiku ndi tsiku. Tikuyang’ana nkhani zofotokozedwa pogwiritsa ntchito zilankhulo za m’madera.

Kujambula Mitengo M’madera pa mapu ndi Kupereka Lipoti la Zaumoyo

Mutha kukonza ntchito yosonkhanitsa ma failo amu kompyuta ku yunivesite kapena ku sukulu kapena m’dera lanu – mwa chitsanzo mungathe kulemba mitundu yosiyanasiyana ya zomera,monga mitengo yomwe ili pafupi ndi inu, kapena kuyeza mmene mpweya ulili kapena mutha kulemba chidziwitso chimene anthu ali nacho chokhudza chilengedwe. Izi zitha kuchitika pogwiritsa ntchito pepala, koma mutha kugwiritsanso ntchito mapulogalamu monga TreeSnap kapena i-Tree polemba mitengo m’madera mwanu, zomwe zingathandize makina amakonowa kutsata mitundu ya mitengo, momwe ilili m’moyo, komanso malo ake.

Kujambula Malo Obiriwira Mothandizidwa ndi Anthu

Nzika zitha kupereka zambiri zokhudzana ndi mapaki a m’madera, minda, ndi madenga obiriwira pogwiritsa ntchito nsanja ngati Green Space Mapper. AI imagwiritsa ntchito deta imeneyi kuti iwonetsetse kusiyanasiyana kwa chilengedwe m’mizinda, kuthandiza pakukonzekera kokonza mizinda, komanso kukulitsa mwayi wofikira zachilengedwe m’madera.

Kuwona ndi Kutsata Zanyama Zakuthengo

Anthu okhala m’mizinda atha kuthandiza kuyang’anira nyama zakuthengo zopezeka m’mizindayo (monga nkhandwe, ma raccoon, ngakhale mbalame zosowa) potumiza zomwe aona kudzera pa mapulogalamu. Zida zoyendetsedwa ndi AI zitha kumatsatabe mitundu zamoyoyi olo patapita nthawi, kuthandiza ofufuza a zinyama zakuthengo kumvetsa bwino machitidwe a chilengedwe m’mizinda.

Mutu umenewu wasankhidwa chifukwa chani?

Mutuwu wasankhidwa chifukwa chakuti dziko limene timathandizira kusamalira komanso kumakhalamo ndi lofunika kwa ife tonse. Kupzolera apo, mutuwu ndi woyenela potengela zochitika zofunikira zotsatirazi zimene zikuchita chaka chino;

  1. Dziko la Malawi ndilapampando wa gulu la Least Developed Countries (LDC) pa za kusintha kwa Nyengo ndipo lidachita msonkhano wa LDC pa 15 ndi 16 April 2025 ku Sunbird Mount Soche Hotel ku Blantyre.
  2. Panopa dziko la Malawi likumalizitsa ndondomeko ya National Biodiversity Strategy and Action Plan imene gwero lake ndi Action Plan II (2015-2025).
  3. Msonkhano wa National Environmental Health and Annual General Meeting, womwe ukuyembekezeka kuchitika kuyambira lachinayi pa 21 August mpaka lachisanu pa 22 August 2025, ku SUNBIRD LIVINGSTONIA HOTEL ku Salima, Malawi.
  4. Dziko la Malawi lili m’gulu la ntchito ya zaka 5 za SBAPP Regional Project ndipo limachitisa msonkhano wapachaka ndi mabungwe ogwira nawo ntchito. Chaka chino msonkhanowu uchitikira ku Salima kumayambiriro kwa mwezi wa June.

Kodi IndabaX Malawi ndi chiyani?

IndabaX Malawi ndi imodzi mwa magawo a Deep Learning Indaba. Idayamba mu chaka cha 2019. Zochitikazi zimachitika chaka chilichonse kupatula mu 2020. Mutha kuwona zambiri zokhudza zochitika zakale pano. Zochitikazi zimafuna kubweretsa pamodzi ofufuza, ophunzira ndi mafakitale omwe ali ndi chidwi chogwiritsa ntchito AI ndi ML kuti athetse mavuto omwe ali m’Malawi. Zochitikazi zakhudza sukulu zaukachenjede zingapo m’Malawi m’zaka zapitazi ndipo zakopa anthu osiyanasiyana.